Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 92:12 - Buku Lopatulika

12 Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa, adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 92:12
17 Mawu Ofanana  

Nakamba za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebanoni kufikira hisope wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwawa pansi ndi za nsomba.


Nalemba m'makoma onse akuzinga chipinda mafano olemba ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, m'katimo ndi kumbuyo kwake.


Ndipo Ayuda anakantha adani ao onse, kuwakantha ndi lupanga, ndi kuwapulula, nachitira odana nao monga anafuna.


Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.


Mitengo ya Yehova yadzala ndi madzi; mikungudza ya ku Lebanoni imene anaioka;


mapiri ndi zitunda zonse; mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse:


Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.


Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi wa azitona m'nyumba ya Mulungu. Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi.


Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.


chakuti pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzaonongeke kosatha.


M'malo mwa mithethe mudzatuluka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamchisu; ndipo chidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati chizindikiro chosatha, chimene sichidzalikhidwa.


Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja ao.


Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwisi; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.


Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m'mwamba, ndi mizu yao pansi.


Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.


Ziyalika monga zigwa, monga minda m'mphepete mwa nyanja, monga khonje wooka Yehova, monga mikungudza m'mphepete mwa madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa