Masalimo 92 - Mawu a Mulungu mu Chichewa ChaleroSalimo 92 Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata. 1 Nʼkwabwino kutamanda Yehova ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba, 2 Kulengeza chikondi chanu mmawa, ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku, 3 kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi ndi mayimbidwe abwino a zeze. 4 Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova; Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu. 5 Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova, maganizo anu ndi ozamadi! 6 Munthu wopanda nzeru sadziwa, zitsiru sizizindikira, 7 kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula, adzawonongedwa kwamuyaya. 8 Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya. 9 Zoonadi adani anu Yehova, zoonadi adani anu adzawonongeka; onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa. 10 Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati; mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga. 11 Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane, makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa. 12 Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa, adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni; 13 odzalidwa mʼnyumba ya Yehova, adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu. 14 Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo, adzakhala anthete ndi obiriwira, 15 kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama; Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.” |
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
Biblica, Inc.