Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 92:5 - Buku Lopatulika

5 Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova, zolingalira zanu nzozama ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova, zolingalira zanu nzozama ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ntchito zanu si kukula kwake, Inu Chauta! Maganizo anu si kuzama kwake!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova, maganizo anu ndi ozamadi!

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 92:5
15 Mawu Ofanana  

Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.


Ntchito za Yehova nzazikulu, zofunika ndi onse akukondwera nazo.


Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri!


Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.


Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.


Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha; chingakhale cha m'kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama.


Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.


Chakutali ndi chakuyadi, adzachipeza ndani?


Ichinso chifumira kwa Yehova wa makamu, uphungu wake uzizwitsa ndi nzeru yake impambana.


Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atachita, mpaka atatha maganizo a mtima wake; masiku otsiriza mudzachidziwa bwino.


Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.


Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa