Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 92:7 - Buku Lopatulika

7 chakuti pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzaonongeke kosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 chakuti pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzaonongeke kosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 ngakhale anthu oipa aziphuka ngati udzu, ndipo anthu ochimwa zinthu ziziŵayendera bwino, kwao nkuwonongeka kwamuyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula, adzawonongedwa kwamuyaya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 92:7
21 Mawu Ofanana  

Mahema a achifwamba akhala mumtendere, ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima; amene Mulungu amadzazira dzanja lao.


Koma olakwa adzaonongeka pamodzi; matsiriziro a oipa adzadulidwa.


Tapenyani, oipa ndi awa; ndipo pokhazikika chikhazikikire aonjezerapo pa chuma chao.


ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu; ndinali ngati nyama pamaso panu.


Anena mau, alankhula zowawa; adzitamandira onse ochita zopanda pake.


Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.


Chifukwa chake okhalamo analefuka, naopsedwa, nathedwa nzeru; ananga udzu wa m'munda, ndi masamba awisi, ndi udzu wa pamatsindwi, ndi munda wa tirigu asanakule.


Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.


Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.


Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa