Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 92:1 - Buku Lopatulika

1 Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nkwabwino kuthokoza Chauta, kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nʼkwabwino kutamanda Yehova ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 92:1
22 Mawu Ofanana  

Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.


Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!


Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!


Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero.


Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.


Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima, oongoka mtima ayenera kulemekeza.


Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.


Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munachichita ichi, ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ichi nchokoma, pamaso pa okondedwa anu.


Ine mwini ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu, ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.


Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.


Ndinati Ine, Inu ndinu milungu, ndi ana a Wam'mwambamwamba nonsenu.


Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu;


ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;


Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.


Momwemo utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa