Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 16:24 - Buku Lopatulika

24 Kufikira tsopano simunapemphe kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Mpaka tsopano simunapemphe kanthu potchula dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 16:24
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isaki, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino:


Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi.


Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israele wakukhala pakati pa akerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wake, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.


Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.


Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzachita.


Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chidzale.


Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa.


Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.


Chisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.


Pokhala ndili nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti chimwemwe chanu chikwanire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa