Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


NDIME ZA CHIKONDI

NDIME ZA CHIKONDI

Tonsefe timafunikira kukondedwa ndipo timafuna kukonda ena, kuyeyambira tili ana timafuna kumva kuti ndife okondedwa, ofunika, komanso othandiza kwa ena. Chikondi ndi mzimu weniweni, wopanda malire, wosafuna kuvulaza wina, koma umangofuna zabwino za mnzake. Ukakhala ndi chikondi umafuna kukonda ena mmene iweyo wakondera, chikondi ndi champhamvu chomwe chimapulumutsa mavuto onse ndipo chimatha kuchita chilichonse, chikondi chimatisintha, chimatilimbikitsa, chimatipangitsa kukhala abwino tsiku ndi tsiku, chikondi chimabweretsa ulemu, kuvomerezana, ndi kuleza mtima.

Mukamachita zabwino zonse mumakhala mukuonetsa chikondi, chifukwa ndi mzimu waukulu umene umabweretsa zabwino zonse kuti zichitike. Chikondi pakati pa anthu awiri chimakhala chobwezerana, zomwe mumamvera munthu wina, nayenso amamvera zomwezo kwa inu. Mtundu wa chikondi umenewu ndi womwe umayambitsa chibwenzi chabwino komanso chopindulitsa. M’Baibulo muli vesi lomwe limafotokoza mmene chikondi chiyenera kukhalira. 1 Akorinto 13: "Chikondi n’choleza mtima, n’chifundo; chikondi sichinyalire, sichidzitamandira, sichidzikuza; sichichita zosayenera, sichitsata zake za icho chokha, sichinyansidwa msanga, sichisunga choipa; sichisangalala ndi chosalungama, koma chisangalala ndi chowonadi".




Ahebri 6:10

pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:40

Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:10

Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:21

Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:9

Koma kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:3

Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 133:1

Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:27

Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:12

Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:13

Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13-14

Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo. Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:34

Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:17

Zinthu izi ndilamula inu, kuti mukondane wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:39

Ndipo lachiwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:14

Zanu zonse zichitike m'chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:9

Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'chikondi changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:16

Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:7

Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:32

Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananene mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:17

Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:8

Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:4-7

Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa; sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:10

Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chili chokwanitsa lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:20-21

Koma inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera, mudzisunge nokha m'chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kufikira moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:14

Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:4-5

Pakuti monga m'thupi limodzi tili nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo sizili nayo ntchito imodzimodzi; chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:34-35

Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli ophunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:13

Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 12:5

Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Mpingo anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:8

koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:32

Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:18

Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:31

Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:26

ndipo ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:2

ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:12

Udani upikisanitsa; koma chikondi chikwirira zolakwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:14

koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:8

Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:44

koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:22

Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:17

Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:10

Iye amene akonda mbale wake akhala m'kuunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:11

Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17-18

Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji? Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:23

Ndipo lamulo lake ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wake Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga anatilamulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:27

Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:14

Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka muimfa kulowa m'moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda akhala muimfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:8

Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:1

Chikondi cha pa abale chikhalebe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:2

Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kuchita malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:20-21

Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone. Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:1-2

Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande. Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera. Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera. Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake. Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu, kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha mu Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu. Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito, mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu; Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:8

Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, muchita bwino:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:12-14

Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho. Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu; ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:14

Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:10

M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:20-21

Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a moto pamutu pake. Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:21-22

Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi? Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 41:1

Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:36

Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 3:12

koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m'chikondano wina kwa mnzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:21

Wolondola chilungamo ndi chifundo apeza moyo, ndi chilungamo, ndi ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:9

Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m'chidziwitso, ndi kuzindikira konse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:165

Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu, landirani ulemerero wonse ndi kutamandidwa, pakuti ndinu nokha woyenera! Mawu anu amati, "Tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu, ndipo aliyense wokonda wabadwa kuchokera kwa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu." Ndikukupemphani kuti muthire chikondi chimenechi pa anjiranga, midzi, mabanja, ndi mitundu yonse ya anthu, kuti tikhale kuwala pakati pa mdima kuti tiyatse ena ndi kuwala kwa Khristu. Kuti tikhale chitsanzo cha utumiki kwa ena, pakuti inu munabwera kudzatumika osati kudzatumikiridwa. Kuchotsa dyera, chiwawa, nkhanza, ndi ulesi. Khazikitsani Ufumu wanu pa mabanja, anjiranga, ndi mitundu yonse. Pakuti ulemerero wonse ndi wanu. M'dzina lamphamvu la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa