Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 41:1 - Buku Lopatulika

1 Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 41:1
27 Mawu Ofanana  

Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.


Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.


Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa, ndipo m'masiku a njala adzakhuta.


Tsiku lonse achitira chifundo, nakongoletsa; ndipo mbumba zake zidalitsidwa.


Wonyoza anzake achimwa; koma wochitira osauka chifundo adala.


Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa; wanzeru adzaukhulula.


Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho.


Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo;


Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m'manja a anthu amene uwaopa.


Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.


M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.


pokhapo kuti tikumbukire aumphawi; ndicho chomwe ndinafulumira kuchichita.


Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.


pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.


Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.


Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza padziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.


Ndipo mpongozi wake ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? Ndi ntchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wake munthu amene anakagwirako ntchito, nati, Dzina lake la munthuyo ndinakagwirako ntchito lero ndiye Bowazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa