Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 41:2 - Buku Lopatulika

2 Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika padziko lapansi, ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi, ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Chauta adzamteteza ndi kumsunga ndi moyo. Adzatchedwa wodala pa dziko. Chauta sadzampereka kwa adani ake, kuti amchite zimene iwo akufuna.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 41:2
16 Mawu Ofanana  

Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa, chifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zachiwawa.


Kupulumutsa moyo wao kwa imfa, ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala.


Pakuti iwo amene awadalitsa adzalandira dziko lapansi; koma iwo amene awatemberera adzadulidwa.


Wachifundo achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake.


Wonyoza anzake achimwa; koma wochitira osauka chifundo adala.


Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho.


Aolowera chikhato chake osauka; natambasulira aumphawi manja ake.


Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m'manja a anthu amene uwaopa.


ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m'mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu ntchito zonse za dzanja lanu muzichitazi.


pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.


Ndipo mpongozi wake ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? Ndi ntchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wake munthu amene anakagwirako ntchito, nati, Dzina lake la munthuyo ndinakagwirako ntchito lero ndiye Bowazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa