Masalimo 41:3 - Buku Lopatulika3 Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Chauta adzamthandiza munthuyo akamadwala. Adzamchiritsa matenda ake onse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda. Onani mutuwo |
Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.