Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 4:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananene mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “Zimene ndiri nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Okhulupirira onse anali a mtima umodzi, ndi maganizo amodzi. Palibe munthu amene amati zomwe anali nazo zinali zake zokha, koma amagawana chilichonse chimene anali nacho.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 4:32
21 Mawu Ofanana  

Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kuchita chowauza mfumu ndi akulu mwa mau a Yehova.


ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;


Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife.


Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.


Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pamalo amodzi.


Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni.


chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina.


Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'chiweruziro chomwecho.


Chotsalira, abale, kondwerani. Muchitidwe angwiro; mutonthozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.


Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;


Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;


akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa