Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -



MAVESI OKHUDZA CHILENGEDWE

MAVESI OKHUDZA CHILENGEDWE

Mulungu ndiye analenga zonsezi. Dziko, thambo, zonse zomwe zili mmenemu, ndi zake. Iye ndiye anazipanga. Monga mmene Baibulo limanenera pa Ekisodo 20:11, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zomwe zili mmenemu m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo anapumula pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. N’chifukwa chake tsiku la Sabata ndi lopatulika. Zonse zimene Mulungu analenga zinali zangwiro, ndipo tiyenera kumutamanda chifukwa cha zodabwitsa zimene anachita.

Tiyeni tiope Mulungu ndi kumupatsa ulemu, chifukwa nthawi ya chiweruzo chake yafika. Tiyeni tilambire iye amene analenga kumwamba, dziko, nyanja, ndi akasupe a madzi. Tiyeni timupatse Mulungu ulemu wonse. Ukakhala pa gombe, ukayang’ana mitengo, kapena mapiri, kumbukira kuti Mlengi wako ndiye anazipanga zokongola ndi zangwiro. Usaleke kupatsa Mulungu ulemu.




Miyambo 12:10

Wolungama asamalira moyo wa choweta chake; koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:9

Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:26

Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:14

Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:26

Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 25:4

Musamapunamiza ng'ombe popuntha tirigu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:23

Udziwitsitse zoweta zako zili bwanji, samalira magulu ako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:9

Amene apatsa zoweta chakudya chao, ana a khwangwala alikulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:5

Ukaona bulu wa munthu wakudana nawe alikugona pansi ndi katundu wake, ndipo ukadaleka kuthandiza, koma uzimthandiza ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:6

Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:10

koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iliyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 65:25

Mmbulu ndi mwanawankhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:6-8

Pita kunyerere, waulesi iwe, penya njira zao nuchenjere; zilibe mfumu, ngakhale kapitao, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe; ndipo zituta dzinthu zao m'masika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:6

Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:24

Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 2:18

Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 4:11

ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:6-7

Mukachipeza chisa cha mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi make alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga make pamodzi ndi ana; muloletu make amuke, koma mudzitengere ana; kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:12

Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 2:15

Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Edeni kuti aulime nauyang'anire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 11:6

Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang'ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 25:7

ndi ng'ombe zako, ndi nyama zili m'dziko lako; zipatso zake zonse zikhale chakudya chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 38:41

Amkonzeratu khwangwala chakudya chake ndani, pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu, naulukauluka osowa chakudya?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 148:10

Nyama zakuthengo ndi zoweta zonse; zokwawa, ndi mbalame zakuuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:11

koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 14:21

Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha; muzipereka icho kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, achidye ndiye; kapena uchigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:10-11

Pakuti zamoyo zonse zakuthengo ndi zanga, ndi ng'ombe za pa mapiri zikwi. Ndidziwa mbalame zonse za m'mapiri, ndipo nyama zakuthengo zili ndi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:11

Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 8:6-8

Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu; mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake; nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo, ndi nyama zakuthengo zomwe; mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja. Zopita m'njira za m'nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 22:28

Koma musamaipha ng'ombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:5

Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:20

Nyama za m'thengo zidzandilimekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; chifukwa ndipatsa madzi m'chipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:34

nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:9

Pakuti m'chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng'ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng'ombe?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:8-9

Sindikudzudzula iwe chifukwa cha nsembe zako; popeza nsembe zako zopsereza zili pamaso panga chikhalire. Sindidzatenga ng'ombe m'nyumba mwako, kapena mbuzi m'makola mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:19

Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 34:15

Kumeneko kadzidzi adzapanga chisa chake, naikira, naumatira, naswa mumthunzi mwake; inde kumeneko miimba idzasonkhana wonse ndi unzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:11-12

Koma Iye anati kwa iwo, Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m'dzenje tsiku la Sabata, kodi sadzaigwira, ndi kuitulutsa? Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Chifukwa cha ichi nkuloleka kuchita zabwino tsiku la Sabata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:27

Izi zonse zikulindirirani, muzipatse chakudya chao pa nyengo yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 39:1

Kodi udziwa nyengo yakuswana zinkhoma? Kodi wapenyerera pakuswa mbawala?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:11

Zimamwamo nyama zonse zakuthengo; mbidzi zipherako ludzu lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:8

Amene aphimba thambo ndi mitambo, amene akonzera mvula nthaka, amene aphukitsa msipu pamapiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 11:7

Ndipo ng'ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao aang'ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng'ombe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:26

Anaankhosa akuveka, atonde aombolera munda;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 38:39

Kodi ukhoza kusakira mkango waukazi nyama? Ndi kukwaniritsa chakudya cha misona,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:33-34

Munthu akafukula dzenje, kapena akakumba dzenje, osalivundikira, ndipo ikagwamo ng'ombe kapena bulu, mwini dzenje azilipa; azilipa ndalama kwa mwini nyamayo, koma yakufayo ndi yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 34:14

Ndidzazidyetsa podyetsa pabwino; ndi pa mapiri aatali a Israele padzakhala kholo lao, apo adzagona m'khola mwabwino, nadzadya podyetsa pokometsera pa mapiri a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:15

Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chao m'nyengo zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 2:19

Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:12

Ndikamva njala, sindidzakuuza, pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwake komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:8

Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula, ndi mlandu wa amasiye onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:24

Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:16

Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:28

Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 29:5

Ndipo ndidzakutaya kuchipululu, iwe ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako; udzagwa kuthengo koyera, sudzaunjikidwa, kapena kuoledwa; ndakupereka ukhale chakudya cha zilombo za padziko, ndi mbalame za kumlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 11:9

Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m'phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:7

Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi! Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 35:11

wakutilangiza ife koposa nyama za padziko, wakutipatsa nzeru zoposa mbalame za m'mlengalenga?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:3

Mbawanso inapeza nyumba, ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake, pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu, mfumu yanga ndi Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 8:1

Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 22:32-33

Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamutu pamaso panga; koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 6:19-20

Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiriziwiri za mtundu wao ulowetse m'chingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi. kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha. Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiriziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:4

Mukapenya bulu kapena ng'ombe ya mbale wanu, zitagwa m'njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:30

Uzitero nazo ng'ombe zako, ndi nkhosa zako; masiku asanu ndi atatu akhale ndi amai wake; tsiku lachisanu ndi chitatu uzimpereka kwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:8-9

Amene aphimba thambo ndi mitambo, amene akonzera mvula nthaka, amene aphukitsa msipu pamapiri. Amene apatsa zoweta chakudya chao, ana a khwangwala alikulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 11:2-3

Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili padziko lapansi. Zokwawa zonse zakuuluka zokhala ndi miyendo inai, muziyesa izi zonyansa. Koma muyenera kudya izi mwa zokwawa zonse zakuuluka, zokhala ndi miyendo inai, zokhala ndi miyendo pa mapazi ao, ya kutumpha nayo pansi; mwa zimenezi muyenera kudya izi: dzombe mwa mtundu wake, ndi chirimamine mwa mitundu yake, ndi njenjete mwa mtundu wake ndi tsokonombwe mwa mitundu yake. Koma zokwawa zonse zakuuluka, za miyendo inai, muziyese zonyansa. Ndipo izi zikudetsani: aliyense akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo aliyense akanyamulako nyama ya mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Nyama iliyonse yakugawanika chiboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; aliyense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa. Ndipo iliyonse iyenda yopanda chiboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; aliyense wokhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo iye amene akanyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa. Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wake; Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:1

Mukapenya ng'ombe kapena nkhosa ya mbale wako zilikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:24-25

Zilipo zinai zili zazing'ono padziko; koma zipambana kukhala zanzeru: Nyerere ndi mtundu wosalimba, koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 17:4

Ndipo kudzakhala kuti uzikamwa mumtsinje, ndipo ndalamulira makwangwala kukudyetsa kumeneko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 7:2-3

Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake. Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri. Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda padziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi, ndi anthu onse: zonse zimene m'mphuno zao munali mpweya wa mzimu wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa. Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali padziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa padziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m'chingalawa. Ndipo anapambana madzi padziko lapansi masiku zana kudza makumi asanu. Ndiponso mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo padziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 13:12

kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:14

koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira ntchito iliyonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena bulu wako, kapena zoweta zako zilizonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wantchito wako wamwamuna ndi wantchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:7

Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:10

Musamalima ndi bulu ndi ng'ombe zikoke pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 8:4-8

munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye? Pakuti munamchepsa pang'ono ndi Mulungu, munamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu. Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu; mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake; nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo, ndi nyama zakuthengo zomwe; mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja. Zopita m'njira za m'nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 9:3-4

Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo. Koma nyama, m'mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:9

Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka, nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 39:19-25

Wampatsa kavalo mphamvu yake kodi? Wamveka pakhosi pake chenjerere chogwedezeka? Ukhoza kodi kuwerenga miyezi yakuzipitira, kapena udziwa nyengo yoti ziswane? Wamlumphitsa kodi ngati dzombe? Ulemerero wa kumina kwake ngwoopsa. Apalasa kuchigwa, nakondwera nayo mphamvu yake; atuluka kukomana nao eni zida. Aseka mantha osaopsedwa, osabwerera kuthawa lupanga. Phodo likuti kochokocho panthiti pake, mkondo wonyezimira ndi nthungo yomwe. Ndi kunjenjemera kwaukali aimeza nthaka, osaimitsika pomveka lipenga. Pomveka lipenga akuti, Hee! Anunkhiza nkhondo ilikudza kutali, kugunda kwa akazembe ndi kuhahaza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:19

Muzisunga malemba anga. Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamavala chovala cha nsalu za mitundu iwiri zosokonezana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:29-31

Pali zinthu zitatu ziyenda chinyachinya; ngakhale zinai ziyenda mwaufulu: Sindinaphunzire nzeru ngakhale kudziwa Woyerayo. Mkango umene uposa zilombo kulimba, supatukira chinthu chilichonse; tambala wolimba m'chuuno, ndi tonde, ndi mfumu yokhala ndi ankhondo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:21

Ndani adziwa mzimu wa ana a anthu wokwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:24

Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 17:14

Pakuti ndiwo moyo wa nyama zonse, mwazi wake ndiwo moyo wake; chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Musamadya mwazi wa nyama iliyonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wake; aliyense akaudya adzachotsedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:3

Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 12:7

Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza, ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:17

Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:14-15

Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka; ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 65:17

Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 39:13-18

Phiko la nthiwatiwa likondwera, koma mapiko ndi nthenga zake nzofatsa kodi? Pakuti isiya mazira ake panthaka, nimafunditsa m'fumbi, nkuiwala kuti phazi lingawaphwanye, kapena chilombo chingawapondereze. Iumira mtima ana ake monga ngati sali ake; idzilemetsa ndi ntchito chabe, popeza ilibe mantha; pakuti Mulungu anaimana nzeru, ndipo sanaigawire luntha. Ikafika nthawi yake, iweramuka, iseka kavalo ndi wa pamsana pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:12

Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo, zimaimba pakati pa mitawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 63:14

Monga ng'ombe zotsikira kuchigwa mzimu wa Yehova unawapumitsa; chomwecho inu munatsogolera anthu anu kudzitengera mbiri yaulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, ulemerero ndi ulemu zikhale kwa Inu! Inu Atate wabwino, Mlengi wa thambo ndi dziko lapansi. Ndikuthokoza kuchokera pansi pa mtima chifukwa cha chilengedwe, zikomo chifukwa chotipatsa chakudya patebulo lathu. Ikani mumtima mwanga chikondi ndi chisamaliro cha dziko lomwe munandipatsa, mundiphunzitse kusamalira chilengedwe chanu. Ndithandizeni kuyamikira ndi kulemekeza miyoyo ya nyama ndi nkhalango. Mawu anu amati: “Thambo ndi lanu, dziko lapansi ndi lanunso; dziko lonse ndi zonse zili mmenemo, inu munalizika.” Tisagwiritse ntchito molakwitsa chilengedwe. Ndikupemphani kuti mundipatse mphamvu zolamulira nyama ndi kusamalira chilengedwe chanu chifukwa ndidzayankha mlandu wake. Ndikupempherera anthu ogwira ntchito yoteteza nyama ndi zomera, amene amateteza zokongola zachilengedwe, mitundu ya nyama yomwe ikutha, ndi amene akugwira ntchito yochepetsa kuipitsidwa kwa dziko. Ndikupempheraninso kuti anthu onse azisangalala ndi chilengedwe ndi zinthu zomwe chimatipatsa mwanzeru ndi modziletsa. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa