Genesis 2:19 - Buku Lopatulika19 Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazicha; ndipo maina omwe onse anazicha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Chauta adatenga dothi naumba nyama zonse ndi mbalame zonse, nabwera nazo kwa Adamu kuti azitche maina. Mwakuti maina amene Adamu adazitcha, maina ake ndi omwewo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake. Onani mutuwo |