Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 104:14 - Buku Lopatulika

14 Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Amameretsa udzu kuti ngʼombe zidye, ndi zomera, kuti munthu azilima kubweretsa chakudya kuchokera mʼdziko lapansi:

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 104:14
18 Mawu Ofanana  

Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula padziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;


Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pamundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.


minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m'thengo:


pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi.


Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.


Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse.


Kunena za nthaka, kuchokera momwemo mumatuluka chakudya, ndi m'munsi mwake musandulizika ngati ndi moto.


kukhutitsa thengo la kunkhwangwala, ndi kuphukitsa msipu?


Ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya; pakuti chifundo chake nchosatha.


Amatuta udzu, msipu uoneka, atchera masamba a kumapiri.


Musamaopa, nyama zakuthengo inu; pakuti m'chipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.


Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.


Ndipo ndidzapatsa msipu wa zoweta zanu podyetsa panu; mudzadyanso nimudzakhuta.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa