Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 6:26 - Buku Lopatulika

26 Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri?

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 6:26
15 Mawu Ofanana  

Ndipo iwe udzitengereko wekha zakudya zonse zodyedwa, nudzisonkhanitsire izi wekha: ndipo zidzakhala zakudya za iwe ndi za iwo.


wakutilangiza ife koposa nyama za padziko, wakutipatsa nzeru zoposa mbalame za m'mlengalenga?


Amkonzeratu khwangwala chakudya chake ndani, pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu, naulukauluka osowa chakudya?


Amene apatsa zoweta chakudya chao, ana a khwangwala alikulira.


Ndidziwa mbalame zonse za m'mapiri, ndipo nyama zakuthengo zili ndi Ine.


Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.


Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wake mkate, adzampatsa mwala?


Ndipo anati Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa