Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 23:12 - Buku Lopatulika

12 Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri musagwire ntchito kuti ngʼombe yanu ndi bulu wanu apume ndiponso kuti kapolo wobadwira mʼnyumba yanu ndi mlendo yemwe apezenso mphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 23:12
13 Mawu Ofanana  

Anakhalanso m'menemo a ku Tiro, obwera nazo nsomba, ndi malonda ali onse, nagulitsa tsiku la Sabata kwa ana a Yuda ndi mu Yerusalemu.


Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa.


koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.


Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, koma lachisanu ndi chiwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula.


Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.


Musamasonkha moto m'nyumba zanu zilizonse tsiku la Sabata.


Amati, Bwanji ife tasala kudya, ndipo Inu simuona? Ndi bwanji ife tavutitsa moyo wathu, ndipo Inu simusamalira? Taonani, tsiku la kusala kudya kwanu inu mupeza kukondwerera kwanu, ndi kutsendereza antchito anu onse.


Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.


Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata;


Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa