Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 23:11 - Buku Lopatulika

11 koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama za kuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wamphesa, ndi munda wako wa azitona.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri muzisiya osalima mindayo kuti anthu osauka pakati panu azipezamo chakudya, ndipo nyama zakuthengo zizidya zotsalazo. Muzichita chimodzimodzi ndi minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 23:11
11 Mawu Ofanana  

ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao pa tsiku la Sabata, kapena tsiku lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse.


Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu;


Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako;


Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.


Ndipo mukadzati, Tidzadyanji chaka chachisanu ndi chiwiri? Taonani, sitidzabzala, sitidzakolola dzinthu;


Ndipo mubzale chaka chachisanu ndi chitatu, ndi kudya zipatso zasundwe; kufikira chaka chachisanu ndi chinai, mpaka zitacha zipatso zake mudzadya zasundwe.


Ndiponso sunatilowetse m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kapena kutipatsa cholowa cha minda, ndi minda yampesa; kodi udzakolowola amuna awa maso ao: Sitifikako.


Popeza waumphawi salekana m'dziko, chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa