Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 20:10 - Buku Lopatulika

10 koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iliyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iliyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 20:10
16 Mawu Ofanana  

ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao pa tsiku la Sabata, kapena tsiku lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse.


Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.


Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.


Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, koma lachisanu ndi chiwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula.


Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.


Pakuti aliyense wa nyumba ya Israele, kapena wa alendo ogonera mu Israele, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ake m'mtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha;


Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.


Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa