Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 20:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iliyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iliyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 20:10
16 Mawu Ofanana  

“Ngati anthu a mitundu ina abwera ndi zinthu za malonda, monga tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la Sabata, sitidzawagula pa tsiku la Sabata kapena pa tsiku lina lililonse loyera. Pa chaka chilichonse cha chisanu ndi chiwiri tidzagoneka munda wosawulima ndipo tidzafafaniza ngongole zonse.


Muzitola chakudya masiku asanu ndi limodzi koma tsiku la chisanu ndi chiwiri ndi la Sabata, simukapeza chilichonse kunjaku.”


“Uza ana a Israeli kuti azisunga Masabata anga. Ichi chidzakhala chizindikiro pakati pa inu ndi Ine pamodzi ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo, chosonyeza kuti Ine ndine amene ndimakuyeretsani.


“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri, musagwire ntchito ina iliyonse, Ngakhale nthawi yolima ndi yokolola muyenera kupuma.


Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku la chisanu ndi chiwiri likhale la Sabata, tsiku lanu lopuma, lopatulika kwa Yehova. Aliyense amene adzagwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuphedwa.


“ ‘Ngati Mwisraeli wina aliyense kapena mlendo wina aliyense wokhala pakati pa Israeli adzichotsa yekha kwa Ine ndi kuyika mtima pa mafano ake ndi kuyikanso maso ake pa zinthu zopunthwitsa ndipo kenaka nʼkupita kwa mneneri kukafunsa nzeru, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha.


“ ‘Pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata lopuma, tsiku la msonkhano wopatulika. Kulikonse kumene inu mukukhala musamagwire ntchito iliyonse tsiku limeneli popeza ndi tsiku la Sabata la Yehova.


Kenaka anapita ku mudzi ndi kukakonza mafuta onunkhira. Koma anapuma pa tsiku la Sabata pomvera malamulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa