Eksodo 20:11 - Buku Lopatulika11 chifukwa m'masiku asanu ndi limodzi Yehova adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 chifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamaliza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera. Onani mutuwo |