Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 10:34 - Buku Lopatulika

34 nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira.

Onani mutuwo Koperani




Luka 10:34
14 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake.


Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.


Ndipo kunali panjira, kuchigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha.


Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m'manda.


Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo,


Ndipo m'mawa mwake anatulutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.


Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.


Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a moto pamutu pake.


Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa