Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 10:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo m'mawa mwake anatulutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo m'mawa mwake anatulutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 M'maŵa mwake adatulutsa ndalama ziŵiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘Msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’

Onani mutuwo Koperani




Luka 10:35
7 Mawu Ofanana  

Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho.


Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola.


Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake.


nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.


Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m'manja a achifwamba?


Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu;


Gayo, mwini nyumba wolandira ine, ndi Mpingo wonse wa Ambuye, akupereka moni. Erasto, ndiye woyang'anira mzinda, akupereka moni, ndiponso Kwarto mbaleyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa