Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 8:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo pa dziko lapansi, naphwa madzi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsono Mulungu adakumbukira Nowa pamodzi ndi nyama zonse zakuthengo ndi zoŵeta zimene zinali naye m'chombomo. Adalamula mphepo kuti iwombe pa dziko lapansi, pomwepo madzi adayamba kutsika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsono Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakuthengo ndi ziweto zimene anali nazo mu chombo. Yehova anatumiza mphepo pa dziko lapansi ndipo madzi anaphwera.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 8:1
35 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene Mulungu anaononga mizinda ya m'chigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chionongeko, pamene anaononga mizinda m'mene anakhalamo Loti.


Ndipo Mulungu anakumbukira Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m'mimba mwake.


ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zotuluka m'chingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi.


Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.


Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.


Muwakumbukire Mulungu wanga, popeza anadetsa unsembe, ndi pangano la unsembe, ndi la Alevi.


ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.


Taona atsekera madzi, naphwa; awatsegulira, ndipo akokolola dziko lapansi.


Ha? Mukadandibisa kumanda, mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.


Popeza anakumbukira mau ake oyera, ndi Abrahamu mtumiki wake.


Mundikumbukire, Yehova, monga momwe muvomerezana ndi anthu anu; mundionetsa chipulumutso chanu:


Yehova watikumbukira; adzatidalitsa: adzadalitsa nyumba ya Israele; adzadalitsa nyumba ya Aroni.


Yehova, kumbukirani Davide kuzunzika kwake konse.


Amene anatikumbukira popepuka ife; pakuti chifundo chake nchosatha.


Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.


Yehova anakhala pa chigumula, inde Yehova akhala mfumu kunthawi yonka muyaya.


Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.


Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum'mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana.


Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza; anamira m'madzi aakulu ngati mtovu.


Ndipo Mulungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.


Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula; chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.


Ndine amene nditi kwa nyanja yakuya, Iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako;


Chilala chili pamadzi ake, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaluka ndi kufuna zoopsa.


Yehova walumbira pali kudzikuza kwa Yakobo, Ngati ndidzaiwala konse ntchito zao zilizonse?


ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?


Adzudzula nyanja, naiphwetsa, naumitsa mitsinje yonse; Basani ndi Karimele afota, ndi duwa la ku Lebanoni linyala.


Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.


Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asiriya kudzagwetsedwa; ndi ndodo yachifumu ya Ejipito idzachoka.


Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.


Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamutu pamaso panga;


Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndi mizinda ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake.


pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira mu Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.


Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wake Hana, Yehova namkumbukira iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa