Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 8:2 - Buku Lopatulika

2 ndipo anatsekedwa akasupe a madzi aakulu ndi mazenera a kumwamba, niletsedwa mvula ya kumwamba;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndipo anatsekedwa akasupe a madzi aakulu ndi mazenera a kumwamba, niletsedwa mvula ya kumwamba;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Akasupe a madzi ambiri okhala pansi pa dziko pamodzi ndi zipata zakuthambo, adazitseka. Mvula adailetsa,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Tsono akasupe a madzi ambiri a pansi pa dziko ndi zitseko za madzi a kumwamba zinatsekedwa, ndipo mvula inaleka kugwa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 8:2
10 Mawu Ofanana  

Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.


Ndipo mvula inali padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku.


Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga padziko lapansi.


Kodi unalowa magwero a nyanja? Kodi unayendayenda pozama penipeni?


Adziwa ndani kuwerenga mitambo mwanzeru, ndi kutsanulira michenje ya kuthambo ndani,


polimbitsa Iye thambo la kumwamba, pokula akasupe a zozama.


Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja, ndipo madzi anandizinga; mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.


Pakuti inenso ndili munthu wakumvera ulamuliro, ndili nao asilikali akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Chita ichi, nachita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa