Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 4:11 - Buku Lopatulika

11 ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mudzi waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Nanga Ine, kodi sindiyenera kuumvera chisoni mzinda waukulu wa Ninive? M'mene mujatu muli anthu opitirira zikwi 120, amene sadziŵa kusiyanitsa kuti zabwino nziti, zoipa nziti, mulinso ziŵeto zochuluka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma mu Ninive muli anthu opitirira 120,000 amene sadziwa kusiyanitsa kuti chabwino nʼchiti ndipo choyipa nʼchiti, mulinso ziweto zochuluka. Kodi sindiyenera kumvera chisoni mzinda waukulu ngati uwu?”

Onani mutuwo Koperani




Yona 4:11
17 Mawu Ofanana  

ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zotuluka m'chingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi.


Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka;


Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.


Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.


Ndipo Senakeribu, mfumu ya Asiriya, anachoka, namuka, nabwerera, nakhala pa Ninive.


Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana choipa ndi kusankha chabwino, dziko limene mafumu ake awiri udana nao lidzasiyidwa.


Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga.


Ndipo Mulungu anaona ntchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka choipa adanenachi kuti adzawachitira, osachichita.


Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirepo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;


kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni?


Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa chabwino kapena choipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa