Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 22:30 - Buku Lopatulika

30 Uzitero nazo ng'ombe zako, ndi nkhosa zako; masiku asanu ndi atatu akhale ndi amai wake; tsiku lachisanu ndi chitatu uzimpereka kwa Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Uzitero nazo ng'ombe zako, ndi nkhosa zako; masiku asanu ndi atatu akhale ndi amai wake; tsiku lachisanu ndi chitatu uzimpereka kwa Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Mundipatsenso ana oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwayo adzangokhala ndi mai wake masiku asanu ndi aŵiri, ndipo mudzampereka kwa Ine pa tsiku lachisanu ndi chitatu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Muchite chimodzimodzi ndi ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwa azikhala ndi amayi ake masiku asanu ndi awiri. Koma pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo muzimupereka kwa Ine.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:30
14 Mawu Ofanana  

A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana aamuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.


kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova.


Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwe, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.


Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera; ndipo musamadziipsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa pansi.


Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndikhale Mulungu wanu; chifukwa chake mukhale oyera, popeza Ine ndine woyera.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adule khungu la mwanayo.


Ndipo aliyense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m'dziko kapena mlendo, azitsuka nsalu zake, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.


Zikamabadwa ng'ombe kapena nkhosa, kapena mbuzi, zikhale ndi make masiku asanu ndi awiri; kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo mwake, idzalandirika ngati chopereka nsembe yamoto ya Yehova.


Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.


Lankhula ndi ana a Israele ndi kuti, Musamadya mafuta ali onse, a ng'ombe, kapena a nkhosa, kapena a mbuzi.


Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi chilombo ayenera ntchito iliyonse, koma musamadya awa konsekonse.


Ndipo musamadya mwazi uliwonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m'nyumba zanu zonse.


Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha; muzipereka icho kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, achidye ndiye; kapena uchigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.


Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng'ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa ntchito yoyamba kubadwa mwa ng'ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa