Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 84:3 - Buku Lopatulika

3 Mbawanso inapeza nyumba, ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake, pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu, mfumu yanga ndi Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Mbawanso inapeza nyumba, ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake, pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu, mfumu yanga ndi Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ngakhale timba amapeza malo okhalapo, nayenso namzeze amamanga chisa chake m'mene amagonekamo ana ake, pafupi ndi maguwa anu, Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo, ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa, kumene amagonekako ana ake pafupi ndi guwa lanu la nsembe, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 84:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inanena ndi Zadoki, Ubwerera nalo likasa la Mulungu kumzindako; akandikomera mtima Yehova, Iye adzandibwezanso, nadzandionetsanso ili, ndi pokhala pake pomwe.


Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako; pakuti Yehova anakuchitira chokoma.


Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?


Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.


Tamvetsani mau a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga; pakuti kwa Inu ndimapemphera.


Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo m'mibadwomibadwo.


Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.


Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m'maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.


Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!


Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa