Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 84:4 - Buku Lopatulika

4 Odala iwo akugonera m'nyumba mwanu; akulemekezani chilemekezere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Odala iwo akugonera m'nyumba mwanu; akulemekezani chilemekezere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ngodala anthu amene amakhala m'Nyumba mwanu, namaimba nyimbo zotamanda Inu nthaŵi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Odala amene amakhala mʼNyumba yanu; nthawi zonse amakutamandani. Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 84:4
13 Mawu Ofanana  

Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova; ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera kunthawi za nthawi.


Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.


Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.


M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.


Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.


Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.


M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu, ndi ulemu wanu tsiku lonse.


Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku mu Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa