1 Akorinto 9:9 - Buku Lopatulika9 Pakuti m'chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng'ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng'ombe? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Pakuti m'chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng'ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng'ombe? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Paja timaŵerenga m'Malamulowo kuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe pamene ikupuntha tirigu.” Kodi pamene adanena zimenezi, Mulungu adangosamala za ng'ombe zokha? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Popeza analemba mʼMalamulo a Mose kuti, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu.” Kodi pamene Mulungu ananena zimenezi ankalabadira za ngʼombe zokha? Onani mutuwo |
koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira ntchito iliyonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena bulu wako, kapena zoweta zako zilizonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wantchito wako wamwamuna ndi wantchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.