Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 12:24 - Buku Lopatulika

24 Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Taonani makwangwala: iwo safesa kapena kukolola, alibe nyumba zosungamo zinthu kapena nkhokwe; komabe, Mulungu amawadyetsa. Koposa kotani inu amene ndi ofunikira kuposa mbalame.

Onani mutuwo Koperani




Luka 12:24
13 Mawu Ofanana  

wakutilangiza ife koposa nyama za padziko, wakutipatsa nzeru zoposa mbalame za m'mlengalenga?


Amkonzeratu khwangwala chakudya chake ndani, pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu, naulukauluka osowa chakudya?


Amene apatsa zoweta chakudya chao, ana a khwangwala alikulira.


Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.


chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.


Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?


Ndipo mfumu inamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo akukhala pachakudya, sanafune kumkaniza.


Ndipo anati Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa.


Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala.


komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa