Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 2:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Nthaŵi imeneyo ndidzachita chipangano ndi nyama zakuthengo, mbalame zamumlengalenga, ndi zokwaŵa pansi, kuti ziyanjane ndi anthu anga. Tsono ndidzathyola uta, lupanga, ndi zida zina zonse zankhondo, ndipo ndidzazichotsa m'dzikomo, kuti iwo apeze moyo wamtendere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga. Ndidzachotsa mʼdzikomo uta, lupanga ndi zida zonse zankhondo, kuti onse apumule mwamtendere.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 2:18
27 Mawu Ofanana  

Chipasuko ndi njala udzaziseka; ngakhale zilombo za padziko osaziopa.


Pakuti udzakhala ndi pangano ndi miyala yakuthengo; ndi nyama zakuthengo zidzakhala nawe mumtendere.


Nyama zakuthengo ndi zoweta zonse; zokwawa, ndi mbalame zakuuluka.


Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha.


Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.


Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.


Ndipo kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, kudzikuza kwa munthu kudzatsitsidwa; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.


Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale makasu; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.


Tsiku limenelo adzaimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tili ndi mzinda wolimba; Iye adzaika chipulumutso chikhale machemba ndi malinga.


Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.


Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.


Mmbulu ndi mwanawankhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.


Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.


Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israele; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutali, ndi mbeu zako kudziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala chete, palibe amene adzamuopsa.


Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzatchedwa nalo, Yehova ndiye chilungamo chathu.


Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.


Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, nenera motsutsana naye Gogi, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Gogi, iwe mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala;


Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo paphiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera.


Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lake ilo lokha.


Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.


Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.


Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa mu Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa mu Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa