Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 2:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo ndidzakutomera ukhale wanga kosatha, inde ndidzakutomera ukhale wanga m'chilungamo, ndi m'chiweruzo, ndi mu ukoma mtima, ndi m'chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo ndidzakutomera ukhale wanga kosatha, inde ndidzakutomera ukhale wanga m'chilungamo, ndi m'chiweruzo, ndi m'ukoma mtima, ndi m'chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Iwe Israele, ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya. Ndidzakutomera mwaungwiro, mwachilungamo, mwa chikondi chosasinthika, ndiponso mwachifundo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya; ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro, mwachikondi ndi mwachifundo.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 2:19
27 Mawu Ofanana  

Chifundo ndi choonadi zakomanizana; chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.


Ziyoni adzaomboledwa ndi chiweruzo, ndi otembenuka mtima ake ndi chilungamo.


M'chilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutali ndi chipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutali ndi mantha, pakuti sadzafika chifupi ndi iwe.


Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.


Pakuti Yehova wakuitana iwe monga mkazi wakusiyidwa ndi wosauka m'mzimu, ngakhale mkazi wa ubwana wochotsedwa, ati Mulungu wako.


Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.


Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.


Ndipo sindidzawabisiranso nkhope yanga, popeza ndatsanulira mzimu wanga pa nyumba ya Israele, ati Ambuye Yehova.


Ndidzachiritsa kubwerera kwao, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wamchokera.


Koma Yuda adzakhala chikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwomibadwo.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wachidetso.


Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.


Chotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Khristu; kuti mukakhale ake a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso.


Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.


Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa