Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


NDIME ZA ZOPEREKA

NDIME ZA ZOPEREKA

Kupereka ndi chinthu chofunika kwambiri, ndipo chimakondweretsa Mulungu wathu. Ukapereka kwa Mulungu, kumbukira kuti upereke zabwino kwambiri zomwe uli nazo, ndi mtima wabwino, wokondwa, ndi wachisangalalo. Mulungu watipatsa zambiri, ngakhale sitikuyenera. Watidalitsa kwambiri. Ukangopereka zotsala zako, dziwa kuti umoyo wako udzakhala womwewo. Tiyenera kupereka ngati tikupereka kwa ife eni, osati mokakamizidwa kapena kuti tibwezeredwe. Tiyenera kupereka popanda kudzitama, osati kuti tiyamikidwe. Dzanja lathu lamanzere lisadziwe zomwe lamanja lichita. Ambuye wathu amakonda wopereka mokondwera, chifukwa amadziwa mitima yathu.

Aliyense apereke monga mmene adaganizira mumtima mwake, osati mopanda chikondi, kapena mokakamizidwa; pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera (2 Akorinto 9:7). Kupereka ndi kugawana zomwe Mulungu watipatsa poyamba, monga chizindikiro chakulambira. Mulungu akapereka, amapereka mochuluka komanso mowolowa mtima. Choncho, tikapereka ndi mtima wonse, timatsegula zitseko kuti Mulungu atipatse zambirimbiri. Ukangopereka mochulukira, ndiye kuti umalandira mochulukira.




Genesis 9:13-15

ndiika utawaleza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi. Ndipo padzakhala pophimba ndi mtambo Ine dziko lapansi, utawo udzaoneka m'mtambomo; ndipo ndidzakumbukira pangano langa limene lili ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo; ndipo madzi sadzakhalanso konse chigumula chakuononga zamoyo zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 15:18

Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 17:7-8

Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako. Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 19:5-6

Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa; ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 24:7-8

Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera. Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati Taonani mwazi wa chipangano, chimene Yehova anachita nanu, kunena za mau awa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:9

Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 9:5

Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 29:9

Chifukwa chake sungani mau a chipangano ichi ndi kuwachita, kuti muchite mwanzeru m'zonse muzichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 30:15-16

Tapenyani, ndaika pamaso panu lero lino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa; popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:10

Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:8

Pakuti Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:31-34

Taonani masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda; si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova. Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga; ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 34:25

Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 36:26-27

Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu. Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 2:5

Chipangano changa chinali naye cha moyo ndi cha mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa chifukwa cha dzina langa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:28

pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:20

Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 8:6-7

Koma tsopano Iye walandira chitumikiro chomveka koposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa. Pakuti loyamba lija likadakhala lopanda chilema sakadafuna malo a lachiwirilo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:15

Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:16-17

Ichi ndi chipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, anena Ambuye: Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba; ndipo machimo ao ndi kusaweruzika kwao sindidzakumbukiranso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:27

Ndipo ichi ndi chipangano changa ndi iwo, pamene ndidzachotsa machimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 12:1-3

Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m'dziko m'menemo. Ndipo panali pamene anayandikira kulowa mu Ejipito, anati kwa Sarai mkazi wake, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako; ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aejipito, adzati, Uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo. Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa cha iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe. Ndipo panali pamene Abramu analowa mu Ejipito, Aejipito anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri. Ndipo akalonga ake a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwake kwa Farao. Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu aakazi, ndi ngamira. Koma Yehova anavutitsa Farao ndi banja lake ndi nthenda zazikulu chifukwa cha Sarai mkazi wake wa Abramu. Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuze ine kuti ndiye mkazi wako? Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke. ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso; Ndipo Farao analamulira anthu ake za iye; ndipo anamperekeza iye m'njira ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo. ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 17:1-2

Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro. Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu. Muzidula khungu lanu; ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa Ine ndi inu. A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana aamuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako. Azidulidwatu amene abadwa m'nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m'thupi mwako pangano losatha. Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa. Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamutcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara. Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amake amitundu, mafumu a anthu adzatuluka mwa iye. Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala? Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, Ha! Ismaele akhale ndi moyo pamaso panu! Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake. Ndipo ndidzapangana pangano langa ndi Ine ndi iwe, ndipo ndidzachulukitsa iwe kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 22:16-18

nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikanize mwana wako, mwana wako yekha, kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:27-28

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israele. Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadye mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:2-3

Yehova Mulungu wathu anapangana nafe chipangano mu Horebu. Usamnamizire mnzako. Usasirire mkazi wake wa mnzako; usakhumbe nyumba yake ya mnzako, munda wake, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako. Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau aakulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa. Ndipo kunali, pamene munamva liu lotuluka pakati pa mdima, potentha phiri ndi moto, munayandikiza kwa ine, ndiwo mafumu onse a mafuko anu ndi akulu anu; ndipo munati, Taonani, Yehova Mulungu wathu anationetsa ulemerero wake, ndi ukulu wake, ndipo tidamva liu lake ali pakati pa moto; tapenya lero lino kuti Mulungu anena ndi munthu, ndipo akhala ndi moyo. Ndipo tsopano tiferenji? Popeza moto waukulu uwu udzatitha. Tikaonjeza kumva mau a Yehova Mulungu wathu, tidzafa. Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife nakhala ndi moyo? Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzichita. Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, pamene munanena ndi ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Ndidamva mau a kunena kwao kwa anthu awa, amene ananena ndi iwe; chokoma chokhachokha adanenachi. Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse! Yehova sanachite chipangano ichi ndi makolo athu, koma ndi ife, ife amene tili ndi moyo tonsefe pano lero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:34

Sindidzaipsa chipangano changa, kapena kusintha mau otuluka m'milomo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:5

Mundisonkhanitsire okondedwa anga, amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 25:1

Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:5

Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 37:26

Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:17-18

Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadze kupasula, koma kukwaniritsa. Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 4:13

Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silinapatsidwe kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake mwa lamulo, koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:15-16

Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo. Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:29

Koma ngati muli a Khristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:122

Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere; odzikuza asandisautse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:17

Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:4-5

Pakuti atero Yehova kwa mifule imene isunga masabata, nisankha zinthu zimene zindikondweretsa Ine, nigwira zolimba chipangano changa, Kwa iyo ndidzapatsa m'nyumba yanga ndi m'kati mwa makoma anga malo, ndi dzina loposa la ana aamuna ndi aakazi; ndidzawapatsa dzina lachikhalire limene silidzadulidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 12:14

Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:10

Ndipo Iye anati, Taona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitike zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:23-24

Dzichenjerani, mungaiwale chipangano cha Yehova Mulungu wanu, chimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, chifaniziro cha kanthu kalikonse Yehova Mulungu wanu anakuletsani. Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:12-13

Ndipo kudzakhala, chifukwa cha kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwachita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani chipangano ndi chifundo chimene analumbirira makolo anu; ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukuchulukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi anaankhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:10

Mayendedwe onse a Yehova ndiwo chifundo ndi choonadi, kwa iwo akusunga pangano lake ndi mboni zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:8

Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la chipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:33

Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:60

Koma ndidzakumbukira Ine pangano langa ndi iwe m'masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:1-2

Chifukwa chake ndinena, Mulungu anataya anthu ake kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndili Mwisraele, wa mbeu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini. maso ao adetsedwe, kuti asapenye, ndipo muweramitse msana wao masiku onse. Chifukwa chake ndinena, Anakhumudwa kodi kuti agwe? Msatero ai; koma ndi kulakwa kwao chipulumutso chinadza kwa anthu akunja, kudzachititsa iwo nsanje. Ndipo ngati kulakwa kwao, kwatengera dziko lapansi zolemera, ndipo kuchepa kwao kutengera anthu amitundu zolemera; koposa kotani nanga kudzaza kwao? Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndili mtumwi wa anthu amitundu, ndilemekeza utumiki wanga; kuti ngati nkutheka ndikachititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena a iwo. Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuyanjanitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakuchokera kwa akufa? Ndipo ngati zipatso zoyamba zili zopatulika, choteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, choteronso nthambi. Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wakuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo, usadzitama iwe wekha pa nthambizo: koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ai, koma muzu ukunyamula iwetu. Ndipo kapena udzanena, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikalumikizidwe nao. Mulungu sanataye anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kapena simudziwa kodi chimene lembo linena za Eliya? Kuti anaumirira Mulungu poneneza Israele, kuti,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 7:22

Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:28

Ndidzamsungira chifundo changa kunthawi yonse, ndipo chipangano changa chidzalimbika pa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:49

Kumbukirani mau a kwa mtumiki wanu, amene munandiyembekezetsa nao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:1-17

Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu. ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya; ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ake pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babiloni. Ndipo pambuyo pake pa kutengedwako ku Babiloni, Yekoniya anabala Sealatiele; ndi Sealatiele anabala Zerubabele; ndi Zerubabele anabala Abihudi; ndi Abihudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro; ndi Azoro anabala Zadoki; ndi Zadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliudi; ndi Eliudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wake wa Maria, amene Yesu, wotchedwa Khristu, anabadwa mwa iye. Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babiloni mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babiloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:72-73

Kuchitira atate athu chifundo, ndi kukumbukira pangano lake lopatulika; chilumbiro chimene Iye anachilumbira kwa Abrahamu atate wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:25

Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 9:4-5

ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira mu Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo; a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:20

Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa Iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:10-14

Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la chilamulo, kuzichita izi. Ndipo chidziwikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu; pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro; koma chilamulo sichichokera kuchikhulupiriro; koma, Wakuzichita izi adzakhala ndi moyo ndi izi. Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo. Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:1

Ndipo chingakhale chipangano choyambachi chinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a padziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:8-9

Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo kumalo opatulika siinaonetsedwe, pokhala chihema choyamba chili chilili; ndicho chiphiphiritso cha kunthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbumtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 26:18

Ndipo Yehova wakulonjezetsani lero kuti mudzakhala anthu akeake a pa okha, monga ananena ndi inu, ndi kuti mudzasunga malamulo ake onse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:19-20

Aonetsa mau ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele. Yehova amanga Yerusalemu; asokolotsa otayika a Israele. Sanatero nao anthu a mtundu wina; ndipo za maweruzo ake, sanawadziwe. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 28:13-15

Taonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isaki; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako; mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa. Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 17:19

Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 30:19-20

Ndichititsa mboni lero, kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu; nimukabwerera kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kumvera mau ake, monga mwa zonse ndikuuzani lero lino, inu ndi ana anu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:14

Ndiye amene akhalitsa malire anu mumtendere; akukhutitsani ndi tirigu wakucha bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:68-69

koma anasankha fuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda. Ndipo anamanga malo oyera ake ngati kaphiri, monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:21

Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 34:24

Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:29

Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso ichi champesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa chatsopano, pamodzi ndi inu, mu Ufumu wa Atate wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:68-69

Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo. Ndipo Iye anatikwezera ife nyanga ya chipulumutso, mwa fuko la Davide mwana wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:39

Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:12-13

Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mgriki; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa Iye; pakuti, aliyense amene adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 9:11

Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamalizidwanso konse ndi madzi a chigumula; ndipo sikudzakhalanso konse chigumula cha kuononga dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 17:4-5

Koma Ine, taona, pangano langa lili ndi iwe, ndipo udzakhala iwe atate wa khamu la mitundu. Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 12:24

Ndipo muzisunga chinthu ichi chikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 111:5

Anapatsa akumuopa Iye chakudya; adzakumbukira chipangano chake kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:6

Amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:12

Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 33:20-21

Pakuti Yehova atero: Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku, m'nyengo yao; pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wake; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 11:19

Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:62

Pakuti ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 4:16

Chifukwa chake chilungamo chichokera m'chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a chilamulo okhaokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:15

Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:4-5

koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo, kuti akaombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 105:9

chipanganocho anapangana ndi Abrahamu, ndi lumbiro lake ndi Isaki;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:18

kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:17

Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadze kupasula, koma kukwaniritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:16

Ichi ndi chipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, anena Ambuye: Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:27

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:37-38

Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakutulutsani pamaso pake ndi mphamvu yake yaikulu, mu Ejipito; kupirikitsa amitundu aakulu ndi amphamvu oposa inu pamaso panu, kukulowetsani ndi kukupatsani dziko lao likhale cholowa chanu, monga lero lino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:30-32

Ana ake akataya chilamulo changa, osayenda m'maweruzo anga, nakaipsa malembo anga; osasunga malamulo anga. Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo, ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:6-7

Kumbukirani, Yehova, nsoni zanu ndi chifundo chanu; pakuti izi nza kale lonse. Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:26-27

ndipo chotero Israele yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti, Adzatuluka ku Ziyoni Mpulumutsi; Iye adzachotsa zamwano kwa Yakobo: Ndipo ichi ndi chipangano changa ndi iwo, pamene ndidzachotsa machimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:26

Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 133:1

Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 136:10-12

Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba; pakuti chifundo chake nchosatha. Natulutsa Israele pakati pao; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka; pakuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:18

Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:18-19

podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu: koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 111:9

Anatumizira anthu ake chipulumutso; analamulira chipangano chake kosatha; dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:10-11

Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake. Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:13

Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadze kudzaitana olungama, koma ochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:27

Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:1-2

Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu; Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake. Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso. Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa. Pakuti kufikira nthawi ya lamulo uchimo unali m'dziko lapansi; koma uchimo suwerengedwa popanda lamulo. Komatu imfa inachita ufumu kuyambira kwa Adamu kufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sanachimwe monga machimwidwe ake a Adamu, ndiye fanizo la wakudzayo. Koma mphatso yaulere siilingana ndi kulakwa. Pakuti ngati ambiriwo anafa chifukwa cha kulakwa kwa mmodziyo, makamaka ndithu chisomo cha Mulungu, ndi mphatso yaulere zakuchokera ndi munthu mmodziyo Yesu Khristu, zinachulukira anthu ambiri. Ndipo mphatso siinadze monga mwa mmodzi wakuchimwa, pakuti mlandu ndithu unachokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere ichokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama. Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inachita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kuchuluka kwake kwa chisomo ndi kwa mphatso ya chilungamo, adzachita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Khristu. Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse. Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama. amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m'chisomo ichi m'mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m'chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 105:8

Akumbukira chipangano chake kosatha, mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:15

Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:3-4

Chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako; Usakangane ndi munthu chabe, ngati sanakuchitire choipa. Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse. Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka. Yehova atemberera za m'nyumba ya woipa; koma adalitsa mokhalamo olungama. Anyozadi akunyoza, koma apatsa akufatsa chisomo. Anzeru adzalandira ulemu cholowa chao; koma opusa adzakweza manyazi. motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:8-9

Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la chipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja; ndi kunena kwa iwo amene ali omangidwa, Mukani, kwa iwo amene ali mumdima, Dzionetseni nokha. Iwo adzadya m'njira, ndi m'zitunda zonse zoti see mudzakhala busa lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 36:28

Ndipo mudzakhala m'dziko ndinapatsa makolo anulo, ndipo mudzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:37

Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:5

Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:142

Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 111:4

Anachita chokumbukitsa zodabwitsa zake; Yehova ndiye wachisomo ndi nsoni zokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:3

Pakuti ndidzathira madzi padziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:7-8

Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu; pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:16-17

Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki. Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:90

Chikhulupiriko chanu chifikira mibadwomibadwo; munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:15

Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:20-21

Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu, akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:47-48

Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu, amene ndiwakonda. Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda; ndipo ndidzalingalira pa malemba anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:2

Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:5

Idzani, muone ntchito za Mulungu; zochitira Iye ana a anthu nzoopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:34-35

Sindidzaipsa chipangano changa, kapena kusintha mau otuluka m'milomo yanga. Ndinalumbira kamodzi m'chiyero changa; sindidzanamizira Davide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:55

Usiku ndinakumbukira dzina lanu, Yehova, ndipo ndinasamalira chilamulo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 9:6

Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:10

Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:45

Ndipo anawakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:3

Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 4:20

ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeke chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m'chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:8

Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:1-5

Lemekeza Yehova, moyo wanga; Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkulukulu; Atumiza akasupe alowe m'makwawa; ayenda pakati pa mapiri: Zimamwamo nyama zonse zakuthengo; mbidzi zipherako ludzu lao. Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo, zimaimba pakati pa mitawi. Iye amwetsa mapiri mochokera m'zipinda zake: Dziko lakhuta zipatso za ntchito zanu. Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka; ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu. Mitengo ya Yehova yadzala ndi madzi; mikungudza ya ku Lebanoni imene anaioka; m'mwemo mbalame zimanga zisa zao; pokhala chumba mpa mitengo ya mikungudza. Mapiri aatali ndiwo ayenera zinkhoma; pamatanthwe mpothawirapo mbira. Anaika mwezi nyengo zake; dzuwa lidziwa polowera pake. muvala ulemu ndi chifumu. Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala; ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga. Muika mdima ndipo pali usiku; pamenepo zituluka zilombo zonse za m'thengo. Misona ya mkango ibangula potsata nyama yao, nifuna chakudya chao kwa Mulungu. Potuluka dzuwa, zithawa, zigona pansi m'ngaka mwao. Pamenepo munthu atulukira kuntchito yake, nagwiritsa kufikira madzulo. Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu. Nyanja siyo, yaikulu ndi yachitando, m'mwemo muli zokwawa zosawerengeka; zamoyo zazing'ono ndi zazikulu. M'mwemo muyenda zombo; ndi Leviyatani amene munamlenga aseweremo. Izi zonse zikulindirirani, muzipatse chakudya chao pa nyengo yake. Chimene muzipatsa zigwira; mufumbatula dzanja lanu, zikhuta zabwino. Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, ndipo zibwerera kufumbi kwao. Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo. Potumizira mzimu wanu, zilengedwa; ndipo mukonzanso nkhope ya dziko lapansi. Ulemerero wa Yehova ukhale kosatha; Yehova akondwere mu ntchito zake; amene apenyerera padziko lapansi, ndipo linjenjemera; akhudza mapiri, ndipo afuka. Ndidzaimbira Yehova m'moyo mwanga: ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo. Pomlingirira Iye pandikonde; ndidzakondwera mwa Yehova. Ochimwa athedwe kudziko lapansi, ndi oipa asakhalenso. Yamika Yehova, moyo wanga. Aleluya. Amene ayesa mphepo amithenga ake; lawi la moto atumiki ake; anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka kunthawi yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, Inu ndinu Alfa ndi Omega! Atate, Mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, Inu ndinu woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi chimaliziro. M'dzina la Yesu, ndimabwera kudzakuthokozani ndi mtima wanga wonse chifukwa cha chikhulupiriro chanu ndi madalitso anu. Mawu anu amati: "Kupatsa kumadalitsa kuposa kulandira". Ambuye Yesu, ndithandizeni kukhala wokoma mtima, kuzindikira zosowa za abale ndi alongo anga, ndithandizeni kukhala chiwonetsero cha chikondi chanu chifukwa chimakondweretsa mtima wanu ndipo ndi nsembe yokondweretsa pamaso panu. Ndipereka mtima wanga kukulemekezani ndi kukutamandani ndi chuma changa, ndi ntchito ya manja anga, pakuti chilichonse chimene ndalandira kuchokera kwa Inu, ndikubwezerani. Lero ndikutsutsa umbombo, kudzikonda, ulesi ndi kusowa chifundo. Ndikupatsani zabwino kwambiri chifukwa Inu munapereka zabwino kwambiri chifukwa cha chikondi chanu kwa ife, landirani nsembe yanga ndipo ikwere ngati fungo labwino pamaso panu. Mawu anu amati: "Amene afesa pang'ono, adzakolola pang'ono, ndipo amene afesa mochuluka, adzakolola mochuluka." Ambuye, momwemonso ndikhale chitoliro cha madalitso ndi kufesa m'miyoyo ya ena, ndipatseni mtima wopatsa ndi wosapsa mtima kuti moyo wanga ukhale nsembe yokondweretsa kwa Inu. Ndimaganiza nthawi zonse ndi chikhulupiriro cholimba kuti mphotho yanga ichokera mu ufumu wakumwamba ndipo chilichonse chimene ndimapereka kwa osowa chili ngati kukupatsani Inu Ambuye wanga. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa