Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 34:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Chauta adauzanso Mose kuti, “Lemba mauŵa, chifukwa potsata mau ameneŵa, ndikuchita chipangano ndi iwe ndi Aisraele onse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba mawu awa pakuti potsatira mawuwa, ine ndipangana pangano ndi iwe ndi Israeli.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 34:27
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.


Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.


Ndipo Iye anati, Taona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitike zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa.


Ndipo Mose analembera chilamulo ichi, nachipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la chipangano la Yehova, ndi kwa akulu onse a Israele.


Pamenepo anakufotokozerani chipangano chake, chimene anakulamulirani kuchichita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa