Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 103:17 - Buku Lopatulika

17 Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa, ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 103:17
27 Mawu Ofanana  

Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.


Chochita Iye ncha ulemu, ndi ukulu: Ndi chilungamo chake chikhalitsa kosatha.


Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.


Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita.


Kumbukirani, Yehova, nsoni zanu ndi chifundo chanu; pakuti izi nza kale lonse.


Chochita Inu chioneke kwa atumiki anu, ndi ulemerero wanu pa ana ao.


ndi kuwachitira chifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi Ine, nasunga malamulo anga.


Koma iwe, Israele, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;


ndiyandikizitsa chifupi chilungamo changa sichidzakhala patali, ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa; ndipo ndidzaika chipulumutso m'Ziyoni, cha kwa Israele ulemerero wanga.


Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi padziko pakuti kumwamba kudzachoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati chofunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa ngati njenjete; koma chipulumutso changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chilungamo changa sichidzachotsedwa.


Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.


Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mzinda wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri.


Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.


Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.


Ndipo ndinena kuti Khristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha choonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,


Koma Yehova anakondwera nao makolo anu kuwakonda, nasankha mbeu zao zakuwatsata, ndiwo inu, mwa mitundu yonse ya anthu, monga kuli lero lino.


amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe,


Simoni Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m'chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa