Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 7:22 - Buku Lopatulika

22 Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Kusiyana kokhudza lumbiroku kukutiwonetsa kuti Yesu ndi Nkhoswe yotsimikizira Chipangano choposa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Chifukwa cha lumbiroli, Yesu wakhala Nkhoswe ya Pangano lopambana.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 7:22
17 Mawu Ofanana  

Ine ndidzakhala chikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, chifukwa chake chidzakhala pa ine masiku onse:


Pakuti kapolo wanu anadziyesa chikole cha mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi chifukwa kwa atate wanga nthawi zonse.


Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere; odzikuza asandisautse.


Tenga malaya a woperekera mlendo chikole; woperekera mkazi wachilendo chikole umgwire mwini.


Mwananga, ngati waperekera mnzako chikole, ngati wapangana kulipirira mlendo,


Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Ambuye ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.


Ndipo iye adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.


pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Ichi ndi mwazi wanga wa chipangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri.


Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.


Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa.


ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.


Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,


Ndipo iwo ndiwo ambiri anakhala ansembe, popeza imfa idawaletsa asakhalebe;


Pakunena Iye, Latsopano, anagugitsa loyambali. Koma chimene chilinkuguga ndi kusukuluka, chayandikira kukanganuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa