Ahebri 9:15 - Buku Lopatulika15 Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Nchifukwa chake Khristu ndi Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti amene Mulungu adaŵaitana, alandire madalitso osatha amene Mulunguyo adalonjeza. Izi zidatheka chifukwa cha imfa ya Khristu, imene imapulumutsa anthu ku zochimwa zozichita akali m'Chipangano choyamba chija. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija. Onani mutuwo |
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.