Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 15:18 - Buku Lopatulika

18 Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pa mtsinje wa ku Ejipito kufikira pa mtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Pa tsiku limeneli mpamene Chauta adachita chipangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapatsa zidzukulu zako dziko lonseli kuyambira ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Pa tsiku limenelo, Yehova anachita pangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako, kuchokera ku mtsinje wa ku Igupto mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 15:18
58 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.


chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse.


Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigrisi: umenewo ndiwo wakuyenda cha kum'mawa kwake kwa Asiriya. Mtsinje wachinai ndi Yufurate.


Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine kunyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.


ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;


akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.


ndipo dziko limene ndinapatsa kwa Abrahamu ndi kwa Isaki ndidzalipatsa kwa iwe ndipo ndidzapatsa mbeu zako za pambuyo pako dzikoli.


Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.


Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu; koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha, lolongosoka mwa zonse ndi losungika; pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse, ndi kufuma kwanga konse, kodi sadzachimeretsa?


Davide anakanthanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wake ku chimtsinje cha Yufurate.


Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake.


Ndipo Hiramu mfumu ya ku Tiro anatuma anyamata ake kwa Solomoni, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m'malo mwa atate wake; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse.


chipanganocho anapangana ndi Abrahamu, ndi lumbiro lake ndi Isaki;


ndi kum'mawa anakhala mpaka polowera kuchipululu kuyambira mtsinje wa Yufurate; pakuti zoweta zao zinachuluka m'dziko la Giliyadi.


Nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero masiku asanu ndi awiri, ndi Aisraele onse pamodzi naye, khamu lalikulu ndithu, kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa ku Ejipito.


Ndipo anthu onse otsala mwa Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, osati Aisraele,


Ndipo analamulira mafumu onse kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti, ndi ku malire a ku Ejipito.


Panalinso mafumu amphamvu mu Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira.


ndipo munampeza mtima wake wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zake; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.


Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani, gawo la cholowa chako;


Ndipo kudzakhala, atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, monga anakulumbirira iwe ndi makolo ako, ndipo anakupatsa ilo,


Ndipo Mulungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.


Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawaononga.


ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.


Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse.


Dzisungire chimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.


Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi.


Ndipo ndinakhazikitsanso nao chipangano changa, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo.


Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova.


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele.


Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


ndipo munawapatsa iwo dziko ili, limene munalumbirira makolo ao kuti mudzawapatsa, dziko moyenda mkaka ndi uchi;


ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere.


pamenepo ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isaki, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukira; ndipo ndidzakumbukira dzikoli.


Koma chifukwa cha iwo ndidzawakumbukira pangano la makolo ao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova.


ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kunka ku mtsinje wa Ejipito, ndi kutuluka kwao adzatuluka kunyanja.


ndipo sanampatse cholowa chake m'menemo, ngakhale popondapo phazi lake iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lake, ndi la mbeu yake yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.


Pamalo ponse padzapondapo phazi lanu ndi panu, kuyambira chipululu ndi Lebanoni, kuyambira pamtsinjewo, mtsinje wa Yufurate, kufikira nyanja ya m'tsogolo, ndiwo malire anu.


Akadzakuza malire a dziko lanu Yehova Mulungu wanu, monga ananena ndi inu, ndipo mukadzati, Ndidye nyama, popeza moyo wanga ukhumba kudya nyama; mudye nyama monga umo monse ukhumba moyo wanu.


Ndipo Yehova Mulungu wanu akakulitsa malire anu, monga analumbirira makolo anu, ndi kukupatsani dziko lonse limene ananena kwa makolo anu kuwapatsa ili;


Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako.


Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;


Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,


kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu;


napitirira ku Azimoni, natuluka ku mtsinje wa Ejipito; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikulu; awa ndi malire anu a kumwera.


nanena kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi wakukhala ndi lipenga, Masula angelo anai omangidwa pamtsinje waukulu Yufurate.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa