Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 37:23 - Buku Lopatulika

23 Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Ngati Yehova akondwera ndi njira ya munthu, amakhazikitsa mayendedwe ake;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:23
19 Mawu Ofanana  

Khazikitsani mapazi anga m'mau anu; ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse.


Ha? Mwenzi zitakhazikika njira zanga kuti ndisamalire malemba anu.


Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzaodzera.


Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.


M'mayendedwe anga ndasunga mabande anu, mapazi anga sanaterereke.


Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.


Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.


Chilungamo chidzamtsogolera; ndipo chidzamkonzera mapazi ake njira.


Muyeso wonyenga unyansa Yehova; koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.


Okhota mtima anyansa Yehova; koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.


Mtima wa munthu ulingalira njira yake; koma Yehova ayendetsa mapazi ake.


Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; njira zako zonse zikonzeke.


Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.


koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.


Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.


Adzasunga mapazi a okondedwa ake, koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima; pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.


Chifukwa chake ulawirire m'mawa pamodzi ndi anyamata a mbuye wako amene anabwera nawe; ndipo mutauka m'mawa, mumuke kutacha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa