Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


MAVESI OKHUDZA MADALITSO

MAVESI OKHUDZA MADALITSO

Madalitso a Mulungu pa moyo wanga amabwera nthawi zonse mokwanira ndipo amafika panthawi yake, sakhala mochedwa. Mulungu amadziwa nthawi yoyenera yotumizira madalitso amene mumapempha m’pemphero.

Tizunguliridwa ndi madalitso okongola a Mulungu, tili ndi thanzi, tili ndi pogona, tili ndi chakudya, tili ndi thanzi la maganizo, tili ndi anthu amene amatikonda ndipo koposa zonse tili ndi Mulungu m’miyoyo yathu, timasangalala ndi mphatso yabwino ya chipulumutso, amenewa ndi madalitso amene nthawi zina sitimazindikira, koma amene anthu ambiri akusowa, ndipo tiyenera kuyamikira zinthu zimenezi, ndi kusangalala chifukwa chifundo cha Mulungu chimakhala chatsopano m’mawa uliwonse.

Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu zonse mogwirizana ndi chuma chake cha ulemerero mwa Khristu Yesu (Afilipi 4:19). Mulungu amalankhula m’mawu ake kuti madalitso ochokera kwa Iye ndi amene amalimbitsa ndipo saonjezera chisoni, Mulungu amadziwa zimene tikufuna ndipo amasamalira ife.

Tikhale oleza mtima kuti madalitso ake adzafika pamene simukuyembekezera. Lambirani Ambuye Mulungu wanu, ndipo adzadalitsa chakudya chanu ndi madzi anu. Ine ndidzachotsa matenda onse pakati panu (Ekisodo 23:25). Khalani ndi moyo womvera Mulungu ndipo madalitso adzabwera nawo.




Mateyu 9:37-38

Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:10

Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:37

Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:35

Kodi simunena inu, kuti, Yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang'ane m'minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:6

Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 67:6

Dziko lapansi lapereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:5

Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru; koma wogona pakututa ndi mwana wochititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:37

nafese m'minda, naoke mipesa, ndiyo yakubala zipatso zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 85:12

Inde Yehova adzapereka zokoma; ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:2

Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:5-6

Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 1:11

Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; chifukwa cha tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 26:3-4

Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita; Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu. Ndipo ndidzasandutsa mizinda yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma. Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako. Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja. Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ake, masiku onse a kupasuka kwake, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ake. Masiku onse a kupasuka kwake lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo. Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola. Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu. Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani. Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo. ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 5:5

Zokolola zao anjala azidya, azitenga ngakhale kuminga, ndi aludzu ameza chuma chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:5

Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 62:8-9

Yehova analumbira padzanja lake lamanja, ndi mkono wake wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira ntchito; koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamtchera adzamumwa m'mabwalo a Kachisi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 5:24

Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yake; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:39

ndipo mdani amene anamfesa uwu, ndiye mdierekezi: ndi kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 10:12

Mudzibzalire m'chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, navumbitsira inu chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 25:4-5

koma chaka chachisanu ndi chiwiri chikhale Sabata lakupumula la dziko, Sabata la Yehova; usamabzala m'munda mwako, usamadzombola mipesa yako. azikhala nawe ngati wolipidwa ntchito, ngati mlendo wako; akutumikire kufikira chaka choliza lipenga. Pamenepo azituluka kukuchokera, iye ndi ana ake omwe, nabwerere ku mbumba yake; abwerere ku dziko laolao la makolo ake. Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo. Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako. Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala a amitundu akuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo aamuna ndi aakazi. Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m'dziko lanu; ndipo adzakhala anuanu. Ndipo muwayese cholowa cha ana anu akudza m'mbuyo, akhale aoao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israele, musamalamulirana mozunza. Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera chuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa fuko la banja la mlendo; atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ake amuombole; kapena mbale wa atate wake, kapena mwana wa mbale wa atate wake amuombole, kapena mbale wake aliyense wa banja lake amuombole; kapena akalemera chuma yekha adziombole yekha. Zophuka zokha zofikira masika usamazithyola, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usazicheka; chikhale chaka chopumula dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 18:12-13

Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa. Zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe. Zipatso zoyamba zonse zili m'dziko mwao, zimene amadza nazo kwa Yehova, zikhale zako; oyera onse a m'banja lako adyeko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:16

ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 24:19

Mutasenga dzinthu zanu m'munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m'mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m'ntchito zonse za manja anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:22

Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 4:29

Pakucha zipatso, pamenepo atenga chisenga, pakuti nthawi yakumweta yafika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:3

Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:8

Wofesa zosalungama adzakolola tsoka; ndipo nthyole ya mkwiyo wake idzalephera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 3:13

Longani chisenga, pakuti dzinthu dzacha; idzani, pondani, pakuti chadzala choponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zao nzazikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 8:22

Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:13

Monga chisanu cha chipale chofewa pa nthawi ya masika, momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma; atsitsimutsa moyo wa ambuyake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 6:11

Akuikidwiratunso nyengo yakukolola, Yuda iwe, pamene ndikabwezanso undende wa anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:30

Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:15

Ndipo mngelo wina anatuluka mu Kachisi, wofuula ndi mau aakulu kwa Iye wakukhala pamtambo, Tumiza chisenga chako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zachetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:18

Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:21-22

Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, koma lachisanu ndi chiwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula. Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 8:20

Masika apita, mphakasa yatha, ndipo ife sitinapulumutsidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:18

Woipa alandira malipiro onyenga; koma wofesa chilungamo aonadi mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 17:11

tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m'mawa mwake; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la chisoni chothetsa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:8

Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:16

Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 16:15

Masiku asanu ndi awiri muchitire Yehova Mulungu wanu madyerero m'malo amene Yehova adzasankha; popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zipatso zanu zonse, ndi m'ntchito zonse za manja anu; nimukondwere monsemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:7

Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:6-8

Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa. Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:23

Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:6

Wam'munda wogwiritsitsa ntchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:17

Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:15

Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 26:12

Ndipo Isaki anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi chaka chimenecho; ndipo Yehova anamdalitsa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:10-11

Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:5

Ndiponso udzalima minda ya mpesa pa mapiri a Samariya; akuoka adzaoka, nadzayesa zipatso zake zosapatulidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 9:13

Taonani, akudza masiku, ati Yehova, akuti wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofetsa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:13

ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukuchulukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi anaankhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:24

Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 4:8

Ndipo zina zinagwa m'nthaka yabwino, ndipo zinapatsa zipatso, ndi kukula ndi kuchuluka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:24-30

Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake; koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole. Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafese mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo? Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wachichita ichi. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi? Koma iye anati, Iai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye. Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu. Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:38

Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:20

Odala muli inu, amene mubzala m'mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng'ombe ndi bulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 6:15

Udzafesa koma osacheka; udzaponda azitona koma osadzola mafuta; udzaponda mphesa koma osamwa vinyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:23-24

Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere mu Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula ya chizimalupsa, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula ya chizimalupsa ndi ya masika mwezi woyamba. Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m'zosungiramo zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:11

Zakudya zikwanira wolima minda yake; koma wotsata anthu opanda pake asowa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:36-38

Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa. Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:8

Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:4

Waulesi salima chifukwa cha chisanu; adzapemphapempha m'masika osalandira kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:12

chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 27:12

Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:24

Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:10-11

Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako; koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:4

Popanda zoweta modyera muti see; koma mphamvu ya ng'ombe ichulukitsa phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:49

Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:18

Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng'ombe yopuntha tirigu. Ndipo Wogwira ntchito ayenera kulipira kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 13:6-9

Ndipo Iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m'munda wake wampesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe. Ndipo anati kwa wosungira munda wampesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake? Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe; ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:1-2

Ndiimbire wokondedwa wanga nyimbo ya wokondedwa wanga ya munda wake wampesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wampesa m'chitunda cha zipatso zambiri; Chifukwa kuti munda wampesa wa madera khumi udzangobala bati imodzi ya vinyo, ndi mbeu za maefa khumi zidzangobala efa imodzi. Tsoka kwa iwo amene adzuka m'mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake. Chifukwa chake anthu anga amuka m'nsinga, chifukwa cha kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi. Ndipo manda akuza chilakolako chake, natsegula kukamwa kwake kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo. Munthu wonyozeka waweramitsidwa, ndi munthu wotchuka watsitsidwa, ndi maso a wodzikweza atsitsidwa; koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'chiweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'chilungamo. Pamenepo anaankhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zachilendo zidzadyapo. Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zachabe, ndi tchimo ngati ndi chingwe cha galeta; amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize ntchito yake kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israele uyandikire, udze kuti tiudziwe! ndipo iye anakumba mcherenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pake nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 4:7

Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mzinda umodzi mvula, osavumbitsira mzinda wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 11:14

Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ake anamva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 12:13

Abzala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:7

Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wantchito ayenera mphotho yake; musachokachoka m'nyumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 7:1

Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wampesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:29

Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako aamuna undipatse Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:11

Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 16:9

Mudziwerengere masabata asanu ndi awiri; muyambe kuwerenga masabata asanu ndi awiri poyambira kusenga tirigu wachilili.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:24-26

Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafese, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaze; ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo. Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafese, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaze;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:24

Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kamvulumvulu awachotsa monga chiputu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:36-38

Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira chobala kumoyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo. Pakuti m'menemo chonenacho chili choona, Wofesa ndi wina, womweta ndi winanso. Ine ndinatuma inu kukamweta chimene simunagwirirapo ntchito: ena anagwira ntchito, ndipo inu mwalowa ntchito yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:10

Kapena achinena ichi konsekonse chifukwa cha ife? Pakuti, chifukwa cha ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugawana nao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:2

mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 6:9

Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israele monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakutchera mphesa m'madengu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 23:10

Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:21-23

pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiike pansi, mututa chimene simunachifese. Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiike, ndi wotuta chimene sindinachifese; ndipo sunapereke bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:4

Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:20

Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pamalo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 37:30

Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe: chaka chino mudzadya zimene zili zomera zokha, ndipo chaka chachiwiri mankhokwe ake; ndipo chaka chachitatu bzalani ndi kudula ndi kulima minda yampesa ndi kudya chipatso chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:41

Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m'dzina langa chifukwa muli ake a Khristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:44

Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:16

M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mizinda adzaphuka ngati msipu wapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:36

Ndipo anati kwa iwo, Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:8

Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 11:6

Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:1-16

Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m'munda wake wampesa. Ndipo m'mene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka. Koma m'mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja, nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake. Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangane ndi ine pa rupiya latheka limodzi? Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe. Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino? Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 28:24-25

Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? Kodi amachocholabe, ndi kuswa zibuma za nthaka? Atakonza thyathyathya pamwamba pake, kodi safesa ponse mawere, ndi kumwazamwaza chitowe, nafesa tirigu m'mizere ndi barele m'malo ake osankhika, ndi mchewere m'maliremo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:14-16

Muzindichitira Ine madyerero katatu m'chaka. Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu; ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:23-25

Ndipo mukadzalowa m'dzikomo, ndi kubzala mitengo ya mitundumitundu ikhale ya chakudya, muziyese zipatso zao monga kusadulidwa kwao; zaka zitatu muziyese zosadulidwa; zisadyedwa. Koma chaka chachinai zipatso zake zonse zikhale zopatulika, za kumlemekeza nazo Yehova. Chaka chachisanu muzidya zipatso zake, kuti zobala zake zikuchulukireni inu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:37-38

nafese m'minda, naoke mipesa, ndiyo yakubala zipatso zambiri. Ndipo awadalitsa, kotero kuti achuluka kwambiri; osachepsanso zoweta zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, Wamuyaya, Wapamwamba! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, woyenera ulemerero wonse ndi kulambiridwa! Lero ndabwera kwa inu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu kuti ndikuyamikireni chifukwa cha kukoma mtima kwanu ndi madalitso onse amene mwandipatsa m'moyo wanga, chifukwa chifuniro chanu ndicho kuti ndizipambana pa chilichonse, kuti inu muonekere mwa ine m'mbali zonse za moyo wanga. Ndithandizeni kuzindikira kuti ngakhale pakati pa mavuto, kudzera mwa Mzimu Woyera wanu ndidzakhala ndi moyo wopambana wodalitsidwa. Inu mwanena m'mawu anu kuti: "Pakuti inu, Yehova, mudzatamanda wolungama; mudzamuzungulira ndi chiyanjo chanu ngati chishango." Zikomo chifukwa mwandikomera mtima mwanjira yapadera, mwandibweretsera machiritso, zosowa zanga, ndi chitetezo m'moyo wanga. Mwandikomera mtima mwa kuyika anthu oyenera pa nthawi yoyenera pa moyo wanga. Chifukwa mwandipangitsa ine kukhala wopambana pa nkhondo zanga zonse, mwandipatsa chigonjetso, chifukwa cha izi ndi zina zambiri, ndikupatsani inu ulemerero wonse. Ambuye ndithandizeni kuti kuposa zonse ndiziphunzira kusunga mtima wanga kuti usakhale wodzikuza ndi wonyada. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa