Amosi 4:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mzinda umodzi mvula, osavumbitsira mzinda wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mudzi umodzi mvula, osavumbitsira mudzi wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 “Ndinenso amene ndidamanga mvula patangotsala miyezi itatu kuti mukolole. Ndine amene ndinkagwetsa mvula pa mudzi wina, koma pa mudzi wina ai. Mvula inkagwa pa munda wina, koma munda wina nkumakhala gwa, chifukwa chosoŵa mvula. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 “Ndinenso amene ndinamanga mvula patangotsala miyezi itatu kuti mukolole. Ndinagwetsa mvula pa mzinda wina, koma pa mzinda wina ayi, mvula inkagwa pa munda wina; koma sinagwe pa munda wina ndipo mbewu zinawuma. Onani mutuwo |