Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 4:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'mizinda yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'midzi yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Ndine amene ndidakusendetsani milomo m'mizinda yanu yonse. Ndine amene ndidagwetsa njala konse kumene munkakhala. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Ndine amene ndinakusendetsani milomo mʼmizinda yanu yonse, ndipo munasowa chakudya mʼmizinda yanu. Komatu inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 4:6
31 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.


Ndipo Eliya ananka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikulu mu Samariya.


Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pake; ndipo anati kwa mnyamata wake, Ika nkhali yaikuluyo, uphikire ana a aneneri.


Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.


Ndipo nthawi ya nsautso yake anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo.


Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.


Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wachotsa ku Yerusalemu ndi ku Yuda mchirikizo wochirikiza chakudya chonse ndi madzi onse, zimene zinali mchirikizo;


Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Koma anthu sanatembenukire kwa Iye amene anawamenya, ngakhale kufuna Yehova wa makamu.


Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mzinda, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.


Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?


Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kuchepsa gawo lako la chakudya, ndi kukupereka ku chifuniro cha iwo akudana nawe, kwa ana aakazi a Afilisti akuchita manyazi ndi njira yako yoipa.


Iye sadzabwerera kunka kudziko la Ejipito, koma Asiriya adzakhala mfumu yake, popeza anakana kubwera.


Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.


Chakudya sichichotsedwa kodi pamaso pathu? Chimwemwe ndi chikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu?


Ndipo mukapanda kulangika nazo ndi kubwera kwa Ine, mukayenda motsutsana ndi Ine;


Pamene ndithyola mchirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mchembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.


Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni ndi matalala m'ntchito zonse za manja anu, koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha.


Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chigololo chake.


Ndipo masiku akuweruza oweruzawo munali njala m'dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu ku Yuda anamuka nakagonera m'dziko la Mowabu, iyeyu, ndi mkazi wake, ndi ana ake aamuna awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa