Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 11:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ake anamva.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ake anamva.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pamenepo adauza mtengowo kuti, “Mtengo iwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya wina aliyense asadzadyekonso zipatso zako.” Mau ameneŵa ophunzira ake aja adaŵamva.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Ndipo Iye anati kwa mtengo, “Palibe amene adzadyenso chipatso kuchokera kwa iwe.” Ndipo ophunzira ake anamva Iye akunena izi.

Onani mutuwo Koperani




Marko 11:14
15 Mawu Ofanana  

Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.


Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wampesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.


Ndipo iye wakugwa pamwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye.


Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.


Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.


Ndipo anaona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m'mene anafikako anapeza palibe kanthu koma masamba okha; pakuti siinali nyengo yake ya nkhuyu.


Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa mu Kachisi, nayamba kutulutsa akugulitsa ndi akugula malonda mu Kachisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;


Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.


Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, akondwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo.


Iye wakukhala wosalungama achitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa; ndi iye wakukhala wolungama achitebe cholungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa