Marko 11:15 - Buku Lopatulika15 Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa mu Kachisi, nayamba kutulutsa akugulitsa ndi akugula malonda mu Kachisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kachisi, nayamba kutulutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kachisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Iwo adafika ku Yerusalemu. Tsono Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa anthu amene ankachita malonda m'menemo. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda, Onani mutuwo |