Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 11:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo anaona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m'mene anafikako anapeza palibe kanthu koma masamba okha; pakuti siinali nyengo yake ya nkhuyu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo anaona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m'mene anafikako anapeza palibe kanthu koma masamba okha; pakuti siinali nyengo yake ya nkhuyu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ataona mkuyu chapatali potero, uli ndi masamba, adapitapo kuti kapena nkupezamo nkhuyu. Koma atafika, sadapezemo nkhuyu, koma masamba okhaokha, pakuti siinali nyengo ya nkhuyu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ataonera patali mtengo wamkuyu uli ndi masamba, anapita kuti akaone ngati unali ndi chipatso chilichonse. Atafika, sanapezemo kanthu koma masamba, chifukwa sinali nthawi ya nkhuyu.

Onani mutuwo Koperani




Marko 11:13
10 Mawu Ofanana  

ndipo iye anakumba mcherenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pake nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya.


Chifukwa kuti munda wampesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.


Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.


Ndipo m'mawa mwake, atatuluka ku Betaniya, Iye anamva njala.


Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ake anamva.


Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina.


Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ochekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Bowazi, ndiye wa banja la Elimeleki.


Ndipo muyang'anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa