Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:44 - Buku Lopatulika

44 Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 “Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m'munda. Munthu wina atachitumba, amachibisanso. Kenaka mokondwa amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula munda uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 “Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:44
29 Mawu Ofanana  

Munthu sadziwa mtengo wake; ndipo silipezeka m'dziko la amoyo.


Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?


Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la chitsiru, popeza wopusa alibe mtima?


Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.


Gula ntheradi, osaigulitsa; nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.


Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndalama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo wake.


Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake;


ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.


Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m'nyanja, ndi kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse;


Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.


Pomwepo Petro anayankha, nati kwa Iye, onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?


Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.


pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.


Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.


Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.


amene zolemera zonse za nzeru ndi chidziwitso zibisika mwa Iye.


Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.


Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.


ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa