Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:45 - Buku Lopatulika

45 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 “Ndiponso Ufumu wakumwamba uli ngati munthu wamalonda wonka nafunafuna ngale zokongola zamtengowapatali.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:45
14 Mawu Ofanana  

Korali kapena ngale sizikumbukikapo. Mtengo wake wa nzeru uposa wa korali wofiira.


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


Chabe zachabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi chabe.


Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake;


ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.


Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?


Koma iwo ananyalanyaza, nachoka, wina kumunda wake, wina kumalonda ake:


Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa