Mateyu 13:46 - Buku Lopatulika46 ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201446 ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa46 Atapeza ngale imodzi yamtengowapatali kwambiri, amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula ngale ija. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero46 Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula.” Onani mutuwo |
malonda a golide, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wake, ndi a ngale, ndi a nsalu yabafuta, ndi a chibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi chotengera chilichonse cha minyanga ya njovu, ndi chotengera chilichonse chamtengo wa mtengo wake wapatali, ndi chamkuwa ndi chachitsulo, ndi chansangalabwi;