Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:47 - Buku Lopatulika

47 Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m'nyanja, ndi kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m'nyanja, ndi kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 “Ufumu wakumwamba ulinso ngati khoka limene anthu amaliponya m'nyanja, ndipo limagwira nsomba za mitundu yonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi khoka limene linaponyedwa mʼnyanja ndipo linakola mitundu yonse ya nsomba.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:47
33 Mawu Ofanana  

Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.


Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.


ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.


limene podzala, analivuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo.


Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.


Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.


ndipo chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, amene anali anzake a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.


Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.


Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.


ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.


Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo ovomerezedwa aonetsedwe mwa inu.


paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mzinda, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;


ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwa Khristu Yesu, kuti akatichititse ukapolo.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa