Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:30 - Buku Lopatulika

30 Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Zilekeni zikulire pamodzi zonse mpaka nyengo yodula. Pa nthaŵi imeneyo ndidzauza odula kuti, Yambani mwazula namsongole, mummange m'mitolo kuti mukamtenthe. Kenaka musonkhanitse tirigu ndi kukamthira m'nkhokwe yanga.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Zisiyeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. Pa nthawi imeneyo ndidzawuza okolola kuti: Poyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga mʼmitolo kuti atenthedwe, kenaka sonkhanitsani tirigu ndi kumuyika mʼnkhokwe yanga.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:30
20 Mawu Ofanana  

koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo; ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao.


Kodi udzaitama kuti itute mbeu zako, ndi kuzisonkhanitsira kudwale?


Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosacheka, ndi dzanja lake lilikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'chigwa cha Refaimu.


Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.


koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.


Koma iye anati, Iai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye.


ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi;


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.


amene chouluzira chake chili m'dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndi kusonkhanitsa tirigu m'nkhokwe yake; koma mankhusu adzatentha m'moto wosazima.


Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Zochimwa za anthu ena zili zooneka kale, zitsogola kunka kumlandu; koma enanso ziwatsata.


Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma Iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga chotuluka m'choponyera mwala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa